Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 12:28-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lace, akuru makumi awiri mphambu awfri.

29. Ndi a ana a Benjamini, abale a Sauli, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ocuruka a iwowa anaumirira nyumba ya Sauli.

30. Ndi a ana a Efraimu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.

31. Ndipo a pfuko la Manase logawika pakati zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ochulidwa maina ao kuti adzalonge Davide mfumu.

32. Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israyeli kuzicita, akuru ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.

33. A Zebuloni akuturuka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida ziri zonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka.

34. Ndi a Nafitali atsogoleri cikwi cimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri.

35. Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.

36. Ndi a Aseri akuturuka kukhamu, akupangira nkhondo, zikwi makumi anai.

37. Ndi tsidya lga la Yordano a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la: Manase logawika pakati, ndi zida: ziri zonse za khamu kucita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri.

38. Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraeli onse; ndi onse otsala a Israyeli omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.

39. Ndipo anali komweko kwa Davide masiku atatu kudya ndi kumwa, popeza abale ao-anazikonzeratu.

40. Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafitali anabwera nao mkate osenzetsa aburu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi ncinci zankhuyu, ndi ncinci zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zocuruka; pakuti munali cimwemwe m'Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 12