Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 12:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mibvi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ace a Sauli, Abenjamini.

3. Mkuru wao ndiye Ahiezeri, ndi Yoasi, ana a Semaa wa ku Gibeya; ndi Yezieli, ndi Peleti, ana a Azmaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti,

4. ndi Ismaya wa ku Gibeoni, wamphamvu mwa makumi atatuwo ndi woyang'anira makumi atatuwo, ndi Yeremiya, ndi Yahazieli, ndi Yohanani, ndi Yozabadi wa ku Gedera,

5. Eluzai, ndi Yerimoti, ndi Bealiya, ndi Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harupi,

6. Elikana, ndi Isiya, ndi Azereli, ndi Yoezeri, ndi Yasobeamu ndiwo Akora;

7. ndi Yoda, ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedoro.

8. Ndi Agadi ena anapambukira kwa Davide ku liogala m'cipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira cikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma kumapiri:

9. Ezeri mkuru wao, waciwiri Obadiya, wacitatu Eliabu,

10. wacinai Misimana, wacisanu Yeremiya,

11. wacisanu ndi cimodzi Atai, wacisanu ndi ciwiri Elieli,

12. wacisanu ndi citatu Yohanani, wacisanu ndi cinai Elzabadi,

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 12