Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 10:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israyeli; ndipo amuna a Israyeli anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa pa phiri la Giliboa.

2. Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Sauli ndi ana ace, ndi Afilistiwo anawapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Sauli.

3. Ndi nkhondoyi inamkulira Sauli, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa cifukwa ca amauta.

4. Pamenepo Sauli anati kwa wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka, Koma wonyamula zida zace anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Sauli anatenga lupanga lace, naligwera.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 10