Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 1:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndi ana a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Rama, ndi Sabteka. Ndi ana a Rama: Seba, ndi Dedani.

10. Ndi Kusi anabala Nimmdi; iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko.

11. Ndi Mizraimu anabala Aludi, ndi Aanami, ndi Alehabi, ndi Anaftuki,

12. ndi Apatrusi, ndi Akasluki, (kumene anafuma Afilisti), ndi Akafitori.

13. Ndi Kanani anabala Zidoni mwana wace woyamba, ndi Heti,

14. ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi,

15. ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini,

16. ndi Aarivadi, ndi Azemari, ndi Ahamati.

17. Ana a Semu: Elamu, ndi Asuri, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu, ndi Uzi, ndi Huli, ndi Geteri, ndi Meseki.

18. Ndi Aripakisadi anabala Sela; ndi Sela anabala Eberi.

19. Ndi Eberi anabala ana amuna awiri, dzina la winayo ndiye Pelegi, popeza masiku ace dziko linagawanika; ndi dzina la mbale wace ndiye Yokitani.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 1