46. Namwalira Husamu; ndi Hadada mwana wa Bedadi, amene anakantha Midyani ku thengo la Moabu, anakhala mfumu m'malo mwace; ndi dzina la mudzi wace ndi Aviti.
47. Namwalira Hadada; ndi Samla wa ku Masereka anakhala mfumu m'malo mwace.
48. Namwalira Samla: ndi Sauli wa ku Rehoboti ku nyanja anakhala mfumu m'malo mwace.
49. Namwalira Sauli; ndi Baalahanani mwana wa Akiboro anakhala mfumu m'malo mwace.
50. Namwalira Baalahanani; ndi Hadada anakhala mfumu m'malo mwace; ndipo dzina la mudzi wace ndi Pai; ndi dzina la mkazi wace ndiye Mehetabele mwana wamkazi wa Matradi mwana wamkazi wa Mezahabu.
51. Namwalira Hadada. Ndipo mafumu a Edomu ndiwo mfumu Timna, mfumu Aliya, mfumu Yeteti;
52. mfumu Oholibama, mfumu Bla, mfumu Pimoni;
53. mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mizibara;
54. mfumu Magadieli, mfumu Iramu. Awa ndi mafumu a Edomu.