23. ndi Ofiri, ndi Havila, ndi Yobabi. Awa onse ndiwo ana a Yokitani.
24. Semu, Aripakisadi, Sela;
25. Eberi, Pelegi, Reu,
26. Serugi, Nahori, Tera;
27. Abramu, (ndiye Abrahamu).
28. Ana a Abrahamu: Isake, ndi Ismayeli.
29. Mibadwo yao ndi awa; woyamba wa Ismayeli Nebayoti; ndi Kedara ndi Adibeli, ndi Mibisamu,
30. Misma, ndi Duma Masa,
31. Hadada, ndi Tema, Nafisi, ndi Kedema. Awa ndi ana a Ismayeli.
32. Ndi ana a Ketura mkazi wamng'ono wa Abrahamu anabala Zimiramu, ndi Yokisani, ndi Medani, ndi Midyani, ndi Isibaki, ndi Sua. Ndi ana a Yokisani: Seba, ndi Dedani.
33. Ndi ana a Midyani: Efa, ndi Eferi, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elidaa. Awa onse ndiwo ana a Ketura.
34. Ndipo Abrahamu anabala Isake. Ana a Isake: Esau, ndi Israyeli.
35. Ana a Esau: Elifazi, Reueli, ndi Yeuzi, ndi Yolamu, ndi Kora.
36. Ana a Elifazi: Teani, ndi Omara, Zefi, ndi Gatamu, Kenazi, ndi Timna, ndi Amaleki.
37. Ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama, ndi Miza.
38. Ndi ana a Seiri: Lotani, ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana, ndi Disoni, ndi Ezeri, ndi Disani.
39. Ndi ana a Lotani: Hori, ndi Homamu; ndipo Timna ndiye mlongo wace wa Lotani.
40. Ana a Sobala: Abiani, ndi Manahati, ndi Ebala, Sefi, ndi Oramu. Ndi ana a Zibeoni: Aiya ndi Ana.