Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 4:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Benabinadabu ku mtunda wa Dori, mkazi wace ndiye Tafati mwana wa Solomo;

12. Baana mwana wa Ahiludi ku Tanaki ndi Megido ndi Betseani konse, ali pafupi ndi Zaratana kunsi kwa Yezreeli, kuyambira ku Betseani kufikira ku Abelimehola, kufikiranso kundunji ku Yokineamu;

13. Benigeheri ku Ramoti Gileadi, iyeyo anali nayo midzi ya Yairo mwana wa Manase iri m'Gileadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobi liri m'Basani, midzi yaikuru makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;

14. Abinadabu mwana wa Ido ku Nahanaimu;

15. Ahimazi ku Nafitali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomo;

16. Baana mwana wa Husayi ku Aseri ndi ku Aloti;

17. Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara;

18. Simeyi mwana wa Ela ku Benjamini;

19. Geberi mwana wa Uri ku dziko la Gileadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m'deramo.

20. Ayuda ndi Aisrayeli anacuruka ngati mcenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 4