Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 21:22-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi ya Basa mwana wa Ahiya; cifukwa ca kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kucimwitsa Israyeli.

23. Ndipo za Yezebeli yemwe Yehova ananena, nati, Agaru adzadya Yezebeli ku linga la Yezreeli.

24. Mwana ali yense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agaru adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya,

25. Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, amene Yezebeli mkazi wace anamfulumiza.

26. Ndipo anacita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazicita Aamori, amene Yehova adawapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.

27. Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli pathupi pace, nasala kudya, nagona paciguduli, nayenda nyang'anyang'a.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 21