Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 15:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2. Anakhala mfumu zaka zitatu m'Yerusalemu, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.

3. Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wace, zimene iye adacita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wace sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide kholo lace.

4. Koma cifukwa ca Davideyo Yehova Mulungu wace anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wace pambuyo pace, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;

5. cifukwa kuti Davide adacita colungama pamaso pa Yehova, osapambuka masiku ace onse pa zinthu zonse adamlamulira iye, koma cokhaco cija ca Uriya Mhiti.

6. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu masiku onse a moyo wace.

7. Ndipo macitidwe ace ena a Abiya, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.

8. Nagona Abiya ndi makolo ace, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wace nalowa ufumu m'malo mwace.

9. Ndipo caka ca makumi awiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.

10. Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu cimodzi, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.

11. Ndipo Asa anacita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 15