Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 14:25-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo kunacitika, Rebabiamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisaki mfumu ya Aigupto anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu,

26. nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; inde anacotsa conseco, nacotsanso zikopa zagolidi zonse adazipanga Solomo.

27. Ndipo mfumu Rehabiamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

28. Ndipo kunacitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku cipinda ca olindirirawo.

29. Tsono, macitidwe ace ena a Rehabiamu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

30. Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku ao onse.

31. Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni, nalowa ufumu m'malo mwace Abiya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 14