Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 14:24-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. panalinso anyamata ocitirana dama m'dzikomo; iwo amacita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapitikitsa pamaso pa ana a Israyeli.

25. Ndipo kunacitika, Rebabiamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisaki mfumu ya Aigupto anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu,

26. nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; inde anacotsa conseco, nacotsanso zikopa zagolidi zonse adazipanga Solomo.

27. Ndipo mfumu Rehabiamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

28. Ndipo kunacitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku cipinda ca olindirirawo.

29. Tsono, macitidwe ace ena a Rehabiamu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

30. Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku ao onse.

31. Nagona Rehabiamu ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amace linali Naama M-amoni, nalowa ufumu m'malo mwace Abiya mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 14