Pakuti cifuniro ca Atate wanga ndi ici, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.