ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupira cifukwa ca kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.