3. ndipo mukapenyerera iye wobvala cokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;
4. kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?
5. Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi cikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonieza kwa iwo akumkonda iye?
6. Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu acuma, nakukokerani iwowa ku mabwalo a mirandu?
7. Kodi sacitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?
8. Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino:
9. koma ngati musamala maonekedwe, mucita ucimo, ndipo mutsutsidwa ndi cilamulo monga olakwa.