1. Koma iwe, lankhula zimene ziyenera ciphunzitso colamitsa:
2. okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'cikhulupiriro, m'cikondi, m'cipiriro.
3. Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa naco cikondi ca pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
4. kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao,
5. akhale odziletsa, odekha, ocita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angacitidwe mwano.
6. Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;