1. PAULO, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Kristu monga mwa cikhulupiriro ca osa nkhika a Mulungu, ndi cizindikiritso ca coonadi ciri monga mwa cipembedzo,
2. m'ciyembekezo ca moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
3. koma pa nyengo za iye yekha anaonetsa mau ace muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:
4. kwa Tito, mwana wanga weni weni monga mwa cikhulupiriro ca ife tonse: Cisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Mpulumutsi wathu.
5. Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;
6. ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.
7. Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;
8. komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;
9. wogwira mau okhulupirika monga mwa ciphunzitso, kuti akakhoze kucenjeza m'ciphunzitso colamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.