7. Koma andilambira Ine kwacabe,Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
8. Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.
9. Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu,
10. Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wakunenera zotpa atate wace kapena amai wace, afe ndithu;
11. koma inu munena, Munthu akati kwa atate wace, kapena amai wace, Karban, ndiko kuti Mtulo, cimene ukadathandizidwa naco ndi ine,
12. simulolanso kumcitira kanthu atate wace kapena amai wace;
13. muyesa acabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzicita.
14. Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:
15. kulibe kanthu kunja kwa munthu kakulowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakuturuka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.[