29. Ndipo anati kwa iye, Cifukwa ca mau amene, muka; ciwanda caturuka m'mwana wako wamkazi.
30. Ndipo anacoka kunka kunyumba kwace, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi ciwanda citaturuka.
31. Ndipo anaturukanso m'maiko a ku Turo, nadzera pakati pa Sidoni, cufikira ku nyanja ya Galileya, ndi cupyola pakati pa maiko a ku Dekapolio
32. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wacibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.
33. Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zace m'makutu mwace, nalabvula malobvu, nakhudza lilime lace:
34. nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Elata, ndiko, Tatseguka.
35. Ndipo makutu ace anatseguka, ndi comangira lilime lace cinamasulidwa, ndipo analankhula cilunjikire.
36. Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu, ali yense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.
37. Ndipo anadabwa kwakukurukuru, nanena, Wacita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.