5. Ndipo Filipo anatsikira ku mudzi wa ku Samarlya, nawalalikira iwo Kristu.
6. Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.
7. Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawaturukira, yopfuula ndi mau akuru; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anaciritsidwa.
8. Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo.
9. Koma panali munthu dzina lace Simoni amene adacita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkuru;
10. ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikuru.
11. Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikuru adawadabwitsa iwo ndi matsenga ace.