Ndipo kunatero kuti atate wace wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namciritsa.