29. Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a cilamulo cao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.
30. Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali ciwembu ca pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.
31. Pamenepo ndipo asilikari, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.
32. Koma m'mawa mwace anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;
33. iwowo, m'mene anafika ku Kaisareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.
34. Ndipo m'mene adawerenga anafunsa acokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Kilikiya,
35. anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba yamlandu ya Herode.