16. Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.
17. Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo.
18. Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo,Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,
19. wotumikira Ambuye ndi kudzicepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;