Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ire pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ire amene tiri Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutiturutsira ire m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atiturutse.