Pamenepo ndinatumiza kwa inu osacedwa; ndipo mwacita bwino mwadza kuno, Cifukwa cace taonani tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.