Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.