Ndipo iwo anati kwa iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawiri kawiri, ndi kucita mapemphero; cimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.