Ndipo anati kwa iwo nthawi yacitatu, Nanga munthuyu anacita coipa ciani? Sindinapeza cifukwa ca kufera iye; cotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula.