1. Ndipo khamu lonselo Iinanyamuka kupita naye kwa Pilato.
2. Ndipo anayamba kumnenera iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu.
3. Ndipo Pilato anamfunsa iye, nanena, Kodindiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo iye anamyankha nati, Mwatero.
4. Ndipo Pilato anati kwa ansembe akuru ndi makamu a anthu, Ndiribe kupeza cifukwa ca mlandu ndi munthu uyu.
5. Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa m'Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.