42. nati, Atate, mukafuna Inu, cotsani cikho ici pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kucitike.
43. Ndipo anamuonekera iye 1 mngelo wa Kumwamba namlimbitsa iye.
44. Ndipo 2 pokhala iye m'cipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lace linakhala ngati madontho akuru a mwazi alinkugwa pansi.
45. Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi cisoni,
46. ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, 3 pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa.
47. Pamene iye anali cilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wochedwa Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona iye.
48. Koma Yesu anati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi cimpsompsono kodi?