Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wace kwa olima mundawo, kuti ampatseko cipatso ca mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.