Ndipo anaitana akapolo ace khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Cita nazoni malonda kufikira ndibweranso.