38. Ndipo anapfuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.
39. Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale cete; koma iye anapfuulitsa cipfuulire, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.
40. Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa iye: ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye,
41. Of una ndikucitire ciani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso.
42. Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.
43. Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anacitira Mulungu mayamiko.