Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.