11. Ndipo pamene pali ponse adzamuka nanu ku mlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena ciani;
12. pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.
13. Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine cuma camasiye.
14. Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?