52. 3 Tsoka inu, acilamulo! cifukwa munacotsa cifungulo ca nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.
53. Ndipo pamene iye anaturuka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza iye kolimba, ndi kumtompha iye ndi zinthu zambiri;
54. 4 namlindira akakole kanthu koturuka m'kamwa mwace.