Zitatha izi ndinao na angelo anai alinkuimirira pa ngondya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse.