Izo ziti nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a cinenero cao; ndipo ulamuliro ziti nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi iri yonse zikafuna.