Ndipo panthawipo panali cibvomezi cacikuru, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi Iidagwa; ndipo anaphedwa m'cibvomezico anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba.