1. Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pace, ndi nkhope yace ngati dzuwa, ndi mapazi ace ngati mizati yamoto;
2. ndipo anali nako m'dzanja lace kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lace lamanja panyanja,
3. ndi Iamanzerelo pamtunda, napfuula ndi mau akuru, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anapfuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.
4. Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo udinamva mau ocokera Kumwamba nanena, Sindikiza naco cizindikilo zimene adalankhula mabingu asanu ndi limodzi, ndipo usazilembe,