22. ndico cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro ca pa Yesu Kristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana;
23. pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;
24. ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa Kristu Yesu;
25. amene Mulungu anamuika poyera akhale cotetezera mwa cikhulupiriro ca m'mwazi wace, kuti aonetse cilungamo cace, popeza Mulungu m'kulekerera kwace analekerera macimo ocitidwa kale lomwe;
26. kuti aonetse cilungamo cace m'nyengo yatsopano; kuti iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu,
27. Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La nchito kodi? lai; koma ndi lamulo la cikhulupiriro.