18. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Kristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asoceretsamitiina ya osalakwa.
19. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Cifukwa cace ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa.
20. Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanva: Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale ndi inu nonse.