Ndi cikhulupiriro Nowa, pocenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pocita mantha, anamanga cingalawa ca kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yace; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa cilungamo ciri monga mwa cikhulupiriro.