20. Ndi cikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zirinkudza,
21. Ndi cikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yace.
22. Ndi cikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anachula za maturukidwe a ana a Israyeli; nalamulira za mafupa ace.
23. Ndi cikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa cilamuliro ca mfumu.
24. Ndi cikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kuchedwa mwana wace wa mwana wamkazi wa Farao;
25. nasankhula kucitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;
26. nawerenga thonzo la Kristu cuma coposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera cobwezera ca mphotho.
27. Ndi cikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika monga ngari kuona wosaonekayo.