7. cotero zindikirani kuti iwo a cikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.
8. Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi cikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.
9. Kotero kuti iwo a cikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo,
10. Pakuti onse amene atama nchito za lamulo Iiwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la cilamulo, kuzicita izi.
11. Ndipo cidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro;
12. koma cilamulo sicicokera kucikhulupiriro; koma, Wakuzicita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.
13. Kristu anatiombola ku temberero la cilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa,Wotembereredwa ali yense woo paeikidwa pamtengo;
14. kutidalitso la Abrahamu mwa Yesu Kristu, licitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa cikhulupiriro.