1. Koma zindikira ici, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.
2. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndarama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
3. osayera mtima, opanda cikondi cacibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,
4. aciwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;