13. Gwira citsanzo ca mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.
14. Cosungitsa cokomaca udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.
15. Ici ucidziwa, kuti onse a m'Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Fugelo ndi Hermogene,
16. Ambuye acitire banja la Onesiforo cifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawiri kawiri, ndipo sanacita manyazi ndi unyolo wanga;
17. komatu pokhala m'Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza,
18. (Ambuye ampatse iye apeze cifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.