14. okhala nao maso odzala ndi cigololo, osakhoza kuleka ucimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
15. posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya cosalungama;
16. koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwace mwini; buru wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyarukakwa mneneriyo.
17. Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene iadima wakuda bii uwasungikira,
18. Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pace, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo;