3. Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,
4. kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;
5. koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;
6. zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;
7. pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azmena, kapena azilimbikirazi.