18. Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;
19. m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,
20. imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka cingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;
21. cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;
22. amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.