Msilikari ndani acita nkhondo, nthawi iriyonse, nadzifunira zace yekha? Aoka mipesa ndani, osadya cipatso cace? Kapena aweta gulu ndani, osadyamkaka wace wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?